Kupeza Choonadi

Phunziro 29

CHIWOMBOLO: Yesu azionetsera kwa ophunzira,nakwera kumwamba

Luka 24:36-53

KUWERENGA MAWU

Kuwerenga ndi kumvetsera mawu. Kubwereza kuwerenga ndi kumvetsera mawu mpaka aliyense atamvetsetsa.

x1.0

Yesu Auka kwa Akufa

24:36Akufotokoza zimenezi, Yesu mwini wake anayimirira pakati pawo ndipo anati, “Mukhale ndi mtendere.”

37Koma chifukwa choti anathedwa nzeru ndi kuchita mantha, ankaganiza kuti akuona mzukwa. 38Iye anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukuvutika? Nʼchifukwa chiyani mukukayika mu mtima mwanu? 39Taonani manja anga ndi mapazi anga. Ine ndine amene! Khudzeni kuti muone. Mzukwa ulibe mnofu ndi mafupa monga mukuonera ndili nazo.”

40Iye atanena izi anawaonetsa manja ake ndi mapazi ake. 41Ndipo pamene iwo samakhulupirirabe, chifukwa cha chimwemwe ndi kudabwa, Iye anawafunsa kuti, “Kodi muli ndi chakudya chilichonse pano?” 42Iwo anamupatsa Iye kachidutswa ka nsomba yophika. 43Iye anakatenga ndi kukadya iwo akuona.

44Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene ndinakuwuzani pamene ndinali nanu: chilichonse chiyenera kukwaniritsidwa chimene chinalembedwa cha Ine mʼbuku la Malamulo a Mose, Aneneri ndi Masalimo.”

45Kenaka anawatsekula maganizo kuti azindikire Malemba. 46Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene zinalembedwa: Khristu adzazunzika ndipo adzauka kwa akufa tsiku lachitatu. 47Ndipo kutembenuka mtima ndi kukhululukidwa kwa machimo zidzalalikidwa mu dzina lake kwa anthu amitundu yonse kuyambira mu Yerusalemu. 48Inu ndinu mboni za zimenezi. 49Ine ndidzakutumizirani chimene Atate anga analonjeza. Koma khalani mu mzinda muno mpaka mutavekedwa mphamvu yochokera kumwamba.”

Kupita Kumwamba

50Iye atawatengera kunja kwa mzindawo mpaka ku Betaniya, anakweza manja ake ndi kuwadalitsa. 51Iye akuwadalitsa, anawasiya ndipo anatengedwa kupita kumwamba. 52Pamenepo anamulambira Iye ndipo anabwerera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu. 53Ndipo iwo anakhalabe ku Nyumba ya Mulungu, akulemekeza Mulungu.

KUFOTOKOZERA

Kufunsa aliyense afotokozere m'mene wamvera mawuwo

ZOYENERA KULINGALIRA


Get it on Google Play
Download on the App Store

Get Discovery Bible Studies on your phone

Discover copyright ©2015-2025 discoverapp.org

Chichewa scriptures from Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™. Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. All rights reserved