Kuwerenga ndi kumvetsera mawu. Kubwereza kuwerenga ndi kumvetsera mawu mpaka aliyense atamvetsetsa.
3:1Ndipo njoka inali yochenjera kuposa nyama yakuthengo iliyonse imene Yehova Mulungu anapanga. Njokayo inati kwa mkaziyo, “Kodi Mulungu ananenadi kuti, ‘Inu musadye zipatso za mtengo uliwonse mʼmundamu?’ ”
2Mkaziyo anati kwa njokayo, “Tikhoza kudya zipatso za mʼmitengo ya mʼmundawu, 3koma Mulungu anati, ‘Musadye zipatso za mu mtengo umene uli pakati pa munda, ndipo musadzawukhudze kuti mungadzafe.’ ”
4“Ndithudi simudzafa,” inatero njokayo kwa mkaziyo. 5“Pakuti Mulungu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye zipatso za mu mtengowo, maso anu adzatsekuka, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wodziwa zabwino ndi zoyipa.”
6Pamene mkaziyo anaona kuti mtengowo unali wabwino kudya ndi wokongola ndi kuti unali wopatsa nzeru, anatengako zipatso zake nadya. Zina anamupatsako mwamuna wake amene anali naye pomwepo ndipo naye anadyanso. 7Kenaka maso awo anatsekuka, ndipo anazindikira kuti anali maliseche. Choncho anasoka masamba a mkuyu nadzipangira zovala.
8Kenaka munthu uja ndi mkazi wake anamva mtswatswa wa Yehova Mulungu akuyendayenda mʼmundamo madzulo a tsikulo, ndipo iwo anabisala pamaso pa Yehova Mulungu pakati pa mitengo ya mʼmundamo. 9Yehova Mulungu anayitana munthu uja kuti, “Uli kuti?”
10Iye anayankha, “Ndinakumvani mʼmundamo, ndipo ndimaopa chifukwa ndinali maliseche; choncho ndinabisala.”
11Ndipo anamufunsa, “Ndani anakuwuza kuti uli maliseche? Kodi wadya zipatso za mtengo umene ndinakulamulira kuti usadye?”
12Koma munthu uja anati, “Mkazi amene munandipatsa kuti ndizikhala nayeyu anandipatsako chipatso cha mtengowo ndipo ndinadya.”
13Tsono Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, “Wachitachi nʼchiyani?”
Mkaziyo anati, “Njoka inandinamiza, ndipo ndinadya.”
14Choncho Yehova Mulungu anati kwa njokayo, “Popeza wachita zimenezi,
“Ndiwe wotembereredwa kuposa ziweto zonse16Kwa mkaziyo Iye anati,
“Ndidzachulukitsa ululu wako kwambiri pamene uli ndi pakati;17Ndipo kwa Adamu Mulungu anati, “Chifukwa wamvera mkazi wako ndipo wadya zipatso za mu mtengo umene ndinakulamulira kuti, ‘Usadye.’
“Nthaka yatembereredwa chifukwa cha iwe,20Munthu uja anatcha mkazi wake Hava, chifukwa iyeyu adzakhala mayi wa anthu onse amoyo.
21Yehova Mulungu anapangira Adamu ndi mkazi wake zovala zachikopa ndipo anawaveka. 22Ndipo Yehova Mulungu anati, “Tsopano munthu uyu wasanduka mmodzi wa ife, wodziwa zabwino ndi zoyipa. Iyeyu asaloledwe kutambasula dzanja ndi kutengako zipatso za mu mtengo wopatsa moyo uja kuti angakhale ndi moyo mpaka muyaya.” 23Kotero Yehova Mulungu anatulutsa Adamu Mʼmunda wa Edeni kuti azilima mʼnthaka imene anachokera. 24Atamuthamangitsa munthu uja, Yehova anayika Akerubi mbali ya kummawa kwa Munda wa Edeni ndi lupanga lamoto limene limayendayenda ponsepo, kuteteza njira ya ku mtengo wopatsa moyo.
Kufunsa aliyense afotokozere m'mene wamvera mawuwo
Get Discovery Bible Studies on your phone
Discover copyright ©2015-2025 discoverapp.org
Chichewa scriptures from Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™. Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. All rights reserved