Kuwerenga ndi kumvetsera mawu. Kubwereza kuwerenga ndi kumvetsera mawu mpaka aliyense atamvetsetsa.
10:25Nthawi ina katswiri wa malamulo anayimirira kuti ayese Yesu. Iye anati, “Aphunzitsi, ndichite chiyani kuti ndikhale ndi moyo wosatha?”
26Yesu anayankha kuti, “Mwalembedwa chiyani mʼMalamulo, ndipo iwe umawerenga zotani?”
27Iye anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse ndi nzeru zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini.”
28Yesu anayankha kuti, “Iwe wayankha bwino, chita zimenezi ndipo udzakhala ndi moyo.”
29Koma iye anafuna kudzilungamitsa yekha, ndipo anamufunsanso Yesu kuti, “Kodi mnansi wanga ndani?”
30Yesu pomuyankha anati, “Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Pa njira anavulazidwa ndi achifwamba. Anamuvula zovala zake, namumenya ndi kuthawa, namusiya ali pafupi kufa. 31Wansembe ankapita pa njira yomweyo, ndipo ataona munthuyo, analambalala. 32Chimodzimodzinso, Mlevi wina pamene anafika pa malopo ndi kumuona, analambalalanso. 33Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, anafika pamene panali munthuyo; ndipo atamuona, anamva naye chisoni. 34Anapita panali munthu wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa zilonda zake, nʼkuzimanga. Kenaka anamukweza pa bulu wake, napita naye ku nyumba ya alendo, namusamalira. 35Mmawa mwake anatenga ndalama ziwiri zasiliva nazipereka kwa woyangʼanira nyumbayo, nati, ‘Musamalireni munthuyu, ndipo pobwera ndidzakubwezerani zonse zimene mugwiritse ntchito.’
36 “Kodi ukuganiza ndi ndani mwa atatuwa, amene anali mnansi wa munthu amene anavulazidwa ndi achifwambawo?”
37Katswiri wa Malamulo uja anayankha kuti, “Amene anamuchitira chifundo.”
Yesu anamuwuza kuti, “Pita, uzikachita chimodzimodzi.”
Marita ndi Mariya
15:11Yesu anapitiriza kunena kuti, “Panali munthu amene anali ndi ana aamuna awiri. 12Wamngʼonoyo anati kwa abambo ake, ‘Abambo, patseni gawo langa la chuma chanu.’ Ndipo iye anawagawira awiriwo chuma chawo.
13 “Pasanapite nthawi, wamngʼonoyo anasonkhanitsa chuma chake chonse, napita ku dziko lakutali ndipo kumeneko anayamba kumwaza chuma chake mʼnjira zachitayiko. 14Iye atawononga zonse, kunagwa njala yoopsa mʼdziko lonselo ndipo anayamba kusauka. 15Iye anapita kwa nzika ina ya dzikolo nakakhala naye ndi kumagwira ntchito, amene anamutumiza ku munda kukadyetsa nkhumba. 16Iye analakalaka atakhutitsa mimba yake ndi makoko amene nkhumbazo zinkadya, koma panalibe wina amene anamupatsa kanthu.
17 “Maganizo ake atabweramo, iye anati, ‘Ndi antchito angati a abambo anga amene ali ndi chakudya chimene amadya nʼkutsalako ndipo ine ndili pano kufa ndi njala! 18Ine ndinyamuka ndi kubwerera kwa abambo anga ndipo ndikati kwa iwo: abambo, ine ndachimwira kumwamba ndi kwa inu. 19Ndine wosayeneranso kutchedwa mwana wanu; munditenge ngati mmodzi wa antchito anu.’ 20Ndipo iye ananyamuka ndi kupita kwa abambo ake.
“Koma iye akanali patali, abambo ake anamuona ndipo anamvera chisoni; anathamangira mwanayo, namukumbatira ndi kupsompsona.
21 “Mwanayo anati, ‘Abambo, ine ndachimwira kumwamba ndi inunso. Ine sindiyenera konse kutchedwa mwana wanu.’
22 “Koma abambowo anati kwa antchito ake, ‘Fulumirani! Bweretsani mkanjo wabwino kwambiri ndipo mumuveke. Muvekeni mphete ndi nsapato. 23Bweretsani mwana wangʼombe wonenepa ndipo iphani. Tiyeni tikhale ndi phwando ndi kukondwerera. 24Pakuti mwana wangayu anali wakufa, ndipo ali ndi moyonso; iye anatayika ndipo wapezeka.’ Chomwecho anayamba kukondwerera.
25 “Nthawi imeneyi, mwana wake wamkulu uja anali ku munda. Iye atafika pafupi ndi nyumba, anamva anthu akuyimba ndi kuvina. 26Ndipo iye anayitana mmodzi wa antchito, namufunsa chimene chimachitika. 27Iye anayankha kuti, ‘Mʼbale wako wabwera ndipo abambo ako apha mwana wangʼombe wonenepa chifukwa wabwera wamoyo ndipo ali bwino.’
28 “Mwana wamkulu anakwiya ndipo anakana kulowa. Chomwecho abambo ake anatuluka ndi kumudandaulira. 29Koma iye anayankha abambo ake kuti, ‘Taonani! Zaka zonsezi ndakhala ndikukutumikirani kugwira ntchito yowawa ndipo palibe pamene sindinamvere malamulo anu. Koma inu simunandipatse ngakhale mwana wambuzi kuti ine ndichite phwando ndi anzanga. 30Koma pamene mwana wanu uyu amene wawononga chuma chanu ndi achiwerewere wabwera ku nyumba, inu mwamuphera mwana wangʼombe wonenepa.’ ”
31 Abambowo anati, “Mwana wanga, iwe umakhala ndi ine nthawi zonse ndipo zonse ndili nazo ndi zako. 32Koma tinayenera kukondwera ndi kusangalala, chifukwa mʼbale wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyonso; iye anali wotayika ndipo wapezeka.”
Kufunsa aliyense afotokozere m'mene wamvera mawuwo
Get Discovery Bible Studies on your phone
Discover copyright ©2015-2025 discoverapp.org
Chichewa scriptures from Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™. Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. All rights reserved