Kupeza Choonadi

Phunziro 21

CHIWOMBOLO: Yesu aphunzitsa kupemphera

Luka 18:9-14; Yohane 16:24

KUWERENGA MAWU

Kuwerenga ndi kumvetsera mawu. Kubwereza kuwerenga ndi kumvetsera mawu mpaka aliyense atamvetsetsa.

x1.0

18:9Yesu ananena fanizoli kwa amene amadzikhulupirira mwa iwo okha kuti anali wolungama nanyoza ena onse. 10“Anthu awiri anapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera, wina Mfarisi ndi winayo wolandira msonkho. 11Mfarisiyo anayimirira ndipo anapemphera za iye mwini kuti, ‘Mulungu, ine ndikuyamika kuti sindili ngati anthu ena onse, achifwamba, ochita zoyipa, achigololo, sindilinso ngati wolandira msonkhoyu. 12Ine ndimasala kudya kawiri pa Sabata ndipo ndimapereka chakhumi pa zonse ndimapeza.’

13 “Koma wolandira msonkhoyo ali chiyimire potero, sanathe nʼkomwe kuyangʼana kumwamba; koma anadziguguda pachifuwa ndipo anati, ‘Mulungu, chitireni chifundo, ine wochimwa.’

14 “Ine ndikukuwuzani kuti munthu wolandira msonkhoyu, osati Mfarisiyu, anapita kwawo atalungamitsidwa pamaso pa Mulungu. Chifukwa chake, aliyense wodzikweza adzachepetsedwa, ndipo wodzichepetsa adzakwezedwa.”

Yesu Adalitsa Ana Aangʼono

16:24Mpaka tsopano simunapemphe kalikonse mʼdzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, ndipo chimwemwe chanu chidzakhala chathunthu.

KUFOTOKOZERA

Kufunsa aliyense afotokozere m'mene wamvera mawuwo

ZOYENERA KULINGALIRA


Get it on Google Play
Download on the App Store

Get Discovery Bible Studies on your phone

Discover copyright ©2015-2026 discoverapp.org

Chichewa scriptures from Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™. Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. All rights reserved