
Kuwerenga ndi kumvetsera mawu. Kubwereza kuwerenga ndi kumvetsera mawu mpaka aliyense atamvetsetsa.
Imfa ndi Kuukitsidwa kwa Lazaro
11:1Tsopano munthu wina dzina lake Lazaro anadwala. Iye anali wa ku Betaniya, mudzi wa Mariya ndi mchemwali wake Marita. 2Mariyayo ndi yemwe uja amene anadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake. Lazaro wodwalayo anali mlongo wake. 3Choncho alongo ake anatumiza mawu kwa Yesu kuti, “Ambuye, uja amene Inu mumamukonda akudwala.”
4Atamva izi, Yesu anati, “Kudwalako safa nako. Koma akudwala kuti Mulungu alemekezedwe; ndi kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe chifukwa cha matendawo.” 5Yesu anakonda Marita, mchemwali wake ndi Lazaro. 6Koma atamva kuti Lazaro akudwala, Iye anakhalabe kumene anali masiku ena awiri.
7Kenaka anati kwa ophunzira ake, “Tiyeni tibwerere ku Yudeya.”
8Ophunzira akewo anati, “Rabi, posachedwa pomwepa Ayuda anafuna kukugendani ndi miyala, koma Inu mukupitanso komweko?”
9Yesu anayankha kuti, “Kodi sipali maora khumi ndi awiri pa tsiku? Munthu amene amayenda masana sapunthwa, popeza akuona chifukwa cha kuwala kwa dziko lapansi. 10Koma amene akuyenda usiku amapunthwa, chifukwa kuwalako alibe.”
11Iye atatha kunena izi, anapitirira kuwawuza iwo kuti, “Bwenzi lathu Lazaro wagona tulo; koma Ine ndikupita kumeneko kukamudzutsa.”
12Ophunzira ake anayankha kuti, “Ambuye, ngati wagona adzapeza bwino.” 13Yesu ankayankhula za imfa yake koma ophunzira ake ankaganiza kuti amanena za tulo chabe.
14Ndipo kenaka anawawuza momveka kuti, “Lazaro wamwalira. 15Ine ndikukondwera chifukwa cha inu kuti kunalibe kumeneko; koma kuti mukakhulupirire tiyeni tipiteko.”
16Pamenepo Tomasi, wotchedwa Didimo, anati kwa ophunzira anzake, “Tiyeni nafenso tipite, kuti tikafere naye pamodzi.”
Yesu Atonthoza Alongo a Lazaro
17Yesu atafika, anapeza kuti Lazaro anali atagona mʼmanda masiku anayi. 18Mudzi wa Betaniya unali pafupi ndi Yerusalemu pa mtunda wosachepera makilomita atatu, 19ndipo Ayuda ambiri anabwera kwa Marita ndi Mariya kudzawatonthoza pa imfa ya mʼbale wawo. 20Pamene Marita anamva kuti Yesu akubwera, anapita kukakumana naye. Koma Mariya anatsala ku nyumba.
21Marita anati kwa Yesu, “Ambuye, mukanakhala muli kuno, mlongo wanga sakanamwalira. 22Koma ine ndikudziwa kuti ngakhale tsopano Mulungu adzakupatsani chilichonse chimene mudzamupempha.”
23Yesu anati kwa iye, “Mlongo wako adzauka.”
24Marita anayankha kuti, “Ine ndikudziwa kuti adzauka pa kuukanso pa tsiku lomaliza.”
25Yesu anati kwa iye, “Ine ndine kuuka ndi moyo. Wokhulupirira Ine, angakhale amwalira adzakhala ndi moyo. 26Aliyense amene ali ndi moyo ndi kukhulupirira Ine sadzamwalira. Kodi iwe ukukhulupirira izi?”
27Marita anamuwuza Iye kuti, “Inde Ambuye, ine ndikukhulupirira kuti ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu, amene abwera mʼdziko lapansi.”
28Ndipo iye atanena izi anabwerera ndi kukayitana mchemwali wake Mariya namuyankhula monongʼona pambali, nati, “Aphunzitsi abwera ndipo akukuyitana.” 29Mariya atamva izi, anayimirira mofulumira napita kwa Iye. 30Tsopano nʼkuti Yesu asanalowe mʼmudzi, koma anali akanali pa malo pamene Marita anakumana naye. 31Ayuda amene ankamutonthoza Mariya mʼnyumba, anaona mmene iye anayimira mofulumira ndi kutuluka kunja, iwo anamutsata akuganizira kuti ankapita ku manda kukalirira kumeneko.
32Mariya anafika pamalo pamene panali Yesu ndipo atamuona, anagwa pa mapazi ake ndipo anati, “Ambuye mukanakhala muli kuno mlongo wanga sakanamwalira.”
33Yesu ataona iye akulira, ndi Ayuda amene anabwera naye akuliranso, anakhudzidwa kwambiri ndi kuvutika mu mzimu. 34Iye anafunsa kuti, “Kodi mwamuyika kuti?”
Iwo anayankha kuti, “Ambuye tiyeni mukaone.”
35Yesu analira.
36Pamenepo Ayuda anati, “Taonani mmene Iye anamukondera Lazaro!”
37Koma ena a iwo anati, “Iye amatsekula maso a munthu wosaona, kodi sakanakhoza kuletsa kuti munthu uyu asamwalire?”
Yesu Aukitsa Lazaro
38Yesu atakhudzidwanso kwambiri anafika ku manda. Manda akewo anali phanga ndipo anatsekapo ndi mwala. 39Yesu anati, “Chotsani mwala.”
Marita mlongo wa womwalirayo anati, “Koma Ambuye, nthawi ino wayamba kununkha, pakuti wakhala mʼmenemu masiku anayi.”
40Kenaka Yesu anati, “Kodi Ine sindinakuwuze kuti ngati iwe ukhulupirira, udzaona ulemerero wa Mulungu?”
41Choncho iwo anachotsa mwalawo. Kenaka Yesu anayangʼana kumwamba ndikuti, “Atate, Ine ndikukuthokozani chifukwa mumandimvera. 42Ine ndimadziwa kuti Inu mumandimvera nthawi zonse, koma Ine ndanena izi chifukwa cha anthu amene ayima pano, kuti iwo akhulupirire kuti Inu munandituma Ine.”
43Yesu atanena izi, Iye anayitana ndi mawu ofuwula kuti, “Lazaro, tuluka!” 44Munthu womwalirayo anatuluka, womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za ku manda, ndi nkhope yake yokulungidwa nsalu.
Yesu anawawuza kuti, “Mʼmasuleni, ndipo muloleni apite.”
Ayuda Apangana za Kupha Yesu
Kufunsa aliyense afotokozere m'mene wamvera mawuwo
Get Discovery Bible Studies on your phone
Discover copyright ©2015-2026 discoverapp.org
Chichewa scriptures from Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™. Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. All rights reserved