
Kuwerenga ndi kumvetsera mawu. Kubwereza kuwerenga ndi kumvetsera mawu mpaka aliyense atamvetsetsa.
20:20Amayi a ana a Zebedayo anabwera ndi ana ake kwa Yesu, nagwada pansi namupempha Iye.
21Yesu anawafunsa kuti, “Mukufuna chiyani?”
Amayiwo anati, “Lolani kuti ana anga awiriwa adzakhale mmodzi ku dzanja lanu lamanja ndi wina ku dzanja lanu lamazere mu ufumu wanu.”
22Yesu anawawuza kuti, “Simukudziwa chimene mukupempha. Kodi mungathe kumwera chikho chimene ndidzamwera Ine?”
Iwo anayankha nati, “Inde tingathe.”
23Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi mudzamwera chikho changa, koma kuti mudzakhale ku dzanja langa lamanja kapena lamazere si kwa Ine kupereka. Malo awa ndi a iwo amene anakonzeredweratu ndi Atate anga.”
24Ophunzira khumi aja, anawapsera mtima abale awiriwo. 25Yesu anawayitana onse pamodzi nati, “Mukudziwa kuti olamulira a mitundu ina ali ndi mphamvu pa iwo, ndipo akuluakulu awo amawalamulira. 26Siziyenera kutero ndi inu. Mʼmalo mwake, aliyense amene akufuna kukhala wamkulu pakati panu akhale wotumikira wanu. 27Ndipo aliyense amene akufuna kukhala woyamba akhale kapolo wanu. 28Momwenso Mwana wa Munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira, ndi kupereka moyo wake kukhala dipo la anthu ambiri.”
Yesu Achiritsa Anthu Awiri Osaona
Kufunsa aliyense afotokozere m'mene wamvera mawuwo
Get Discovery Bible Studies on your phone
Discover copyright ©2015-2026 discoverapp.org
Chichewa scriptures from Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™. Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. All rights reserved